Bungwe la Greenbelt Authority lati ndi lokhutitsidwa ndi kuchulukwa kwa chimanga chomwe bungweli lalima ku imodzi mwa ma Mega Farm ya Chikwawa Irrigation Scheme m’boma la Salima.
Malinga ndi mkulu owona zaulimi kubungweli, a Gideon Zumani, pali chiyembekezo kuti akolola chimanga chochuluka kwambiri pamalowa, amenenso ali kufupi ndi factory ya Salima Sugar.
Pali chiyembekezo kuti zimenezi zithandiziranso kuti mtengo wa chimanga, umene wayamba kale kutsika mmadera ena monga m’boma la Lilongwe, ukhale ukupitirira kukhala okomera anthu a m’dziko muno.
A Zumani akufotokoza mukanemayu.
https://web.facebook.com/reel/2110272176099762