Timu ya Silver Strikers, yomwe ikuteteza ukatswiri waligi ya TNM, yagonja 1-0 ndi FCB Nyasa Big Bullets pamasewero amene anali pa bwalo lamasewero la Bingu munzinda wa Lilongwe.
Babatunde Adepoju ndiye adamwetsa chigoli cha Bullets patatha mphindi 30 m’chigawo choyamba cha masewerowa.
Mphunzitsi wa Bullets, a Peter Mponda, anayamikira osewera ake kaamba kogwira ntchito yotamandika ndipo anati akonza mavuto ena omwe waona m’masewerowa.
Mbali inayi, mphunzitsi wa Silver Strikers, a Peter Mgangira, anati ndi okhutira ndi momwe osewera ake ayamabira masewerawa, ngakhale agonja.
Pakadali pano, timu ya Bullets ili panambala yachiwiri pa mndandanda wa matimu a ligiyi pomwe Silver ili panambala 15.
Ekhaya, yomwe yangolowa kumene ligiyi, ndi yomwe ili pachiongolero itathambitsa ndi kugonjetsa Mighty Tigers 2-0 munzinda wa Blantyre.