Gulu loimba mingoli yauzimu m’dziko muno la The Harps laitana makwaya aku Zambia ndi Zimbabwe pachikondwerero cha zaka khumi zamaimbidwe pomwenso likukhazikitsa chimbale chatsopano.
Makwaya awiriwa ndi Redeemed Family yaku Zimbabwe ndi Sovereign Family yaku Zambia omwe afika m’dziko muno kudzera pabwalo la ndege la Kamuzu ku Lilongwe.
Malinga ndi Owen Nkoka, wapampando wagulu la The Harp, mwambowu uchitika la Mulungu pa BICC mnzinda wa Lilongwe ndipo anthu ayembekezere kutsitsimuka ndi kuona maimbidwe apamwamba.
Wapampando wagulu laku Zimbabwe wati kupatula kuthandiza gulu la m’dziko munoli kwayayi ikuyembekezeka kuimbanso ndi oimba nyimbo zauzimu akuno ku Malawi.
Olemba: Emmanuel Chikonso