Phungu wadera la Kumachenga m’boma la Lilongwe a Ezra Ching’onga adandaula kuti ophunzira ambiri omwe amalemba mayeso a MSCE mdera lake sasankhidwa kupita ku university chifukwa amalephera kusankha moyenera ma programme aku university mogwirizana ndi momwe akhonzera mayeso a MSCE.
“Ophunzira mdera lathu amakhonza mayeso a MSCE koma sapita ku sukulu zaukachenjede. Chitsanzo ena amakhoza ndi ma points oposa makumi awiri, koma akufuna maphunziro azasayansi monga engineering, a NCHE angamutenge ?” anadandaula choncho a Ching’onga.
Iwo anati kusankha moyenera kungatheke ndi thandizo la aphunzitsi komanso makolo amene ali ndikuthekera.
Iwo ayankhula izi pamwambo otsanzikana ndi ophunzira a Form 4 apa sukulu ya Njewa Community Day.
Mphunzitsi wamkulu pa sukulupo a Emmanuel Mponda ati ayesetsa kuwunikila achinyamatawo pa zisankho zoyenera.