Nduna ya zokopa alendo a Vera Kamtukule omwe anali achipani cha UTM alowa chipani cha Malawi Congress.
Powalandira mchipanichi Mlembi Wamkulu mchipani cha MCP a Eisenhower Mkaka ati a Kamtukule sanasochere kaamba koti alowa chipani chomwe chilibe mwini koma mchipani cha m’Malawi aliyense.
A Mkaka ati chipani cha MCP chili chokonzeka kulandira aliyense yemwe watsimikiza mtima kulowa chipanichi.
Poyankhulapo a Kamtukule ati alowa chipanichi kaamba koti akufuna kuthandiza mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwera pogwira ntchito yotukula dziko la Malawi.