Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Michael Usi wamema a Malawi kuti adzipempherera mtsogoleri wathu Dr Lazarus Chakwera komanso a Mary Chilima pa nthawi yomwe dziko lino likhuza imfa ya Dr Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu omwe anatisiya pa ngozi ya ndege munkhalango ya Chikangawa m’boma la Mzimba pa 10 June 2024.
Dr Usi amalankhula izi m’boma la Mulanje pa tchalitchi cha CCAP cha Mulanje Mission kumene anakachita nawo mapemphero.
Iwo anati akudziwa kuti a Malawi akulankhula zambiri zokhudza imfa ya Dr Chilima komabe anati ndi kofunika kuti mpingo komanso akhristu apitirize kuwapempherera.
“Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuyimanga, ayimanga chabe,” a Usi anatero.
Poyankhulapo, Moderator wa wa Mulanje Mission CCAP, m’busa Innocent Brave Chikopa, anati mapempherowa anawakonza pofuna kukumbukira imfa ya malemu Dr Chilima ndi ena asanu ndi atatu.
A Chikopa anatinso kutenga nawo mbali kwa Dr Usi pa mapempherowa kunalinso kufuna chitsogozo cha Mulungu pamene akhale akuyamba kugwira ntchito yawo ngati wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino.
Mu ulaliki wawo, iwo analalikira pa mutu oti kusankha chikhulupiliro m’katikati mwa mavuto.
Senior Chief Chikumbu, amene anali nawo pa mapempherowa, anafunira zabwino Dr Usi pamene akukayamba ntchito yawo.
Olemba: Mercy Zamawa