Ntchito yogawa chimanga chaulere kwa anthu ovutika yomwe akuchita mtsogoleri wa mpingo wa Enlightened Christian Gathering the Jesus Nation Prophet Shepherd Bushiri ipitilira nchigawo chakummwera kumathero asabatayi mmaboma a Mulanje ndi Thyolo.
Pakadali pano anthu okwana 24000 ndi omwe alandira kale thandizoli m’maboma a Ntcheu ndi Lilongwe.
Polankhula pomwe amakagawa chimangachi m’maboma a Ntcheu ndi Lilongwe, Prophet Bushiri anati nkofunika kuti anthu akufuna kwabwino omwe ali ndi kochepa, agawireko ena powonetsa chikondi chomwe Mulungu amatiphunzitsa.
Lipoti la MVAC, yemwe ndi kafukufuku wa mmene chakudya chikupezekera m’dziko muno linaonetsa kuti anthu opitilira 4 million ndi omwe akhudzidwa ndi njala chaka chino mdziko muno.
Olemba: Eunice Ndhlovu.
#mbconlineservices