Boma lakhazikitsa gawo lachiwiri la ntchito yolimbikitsa mtendere komanso kumverana pa mwambo umene unachitikira m’mudzi mwa mfumu yayikulu Mphonde m’boma la Nkhotakota.
Komishoni ya Malawi Peace and Unity, molumikizana ndi nthambi za UNFPA, UNDP komanso IOM ndi amene agwire ntchitoyi ndi thandizo lochokera m’dziko la Ireland.
Cholinga chake ndi chakuti mtendere, chilungamo komanso magulu obweretsa bata adzilimbikitsa anthu kukhala mololerana m’madera a maboma amene ali m’malire a dziko lino, zimene ndi zogwirizana ndi masomphenya amayiko, kuphatikizirapo dziko lino, pa mfundo zachitukuko.
Mayikowa ati akuyenera kulimbikitsa mtendere komanso chilungamo pofika chaka cha 2030.
Nduna yoona za achinyamata komanso masewero, a Uchizi Mkandawire, ati kukhazikitsa ntchitoyi ndi kofunikira kwambiri chifukwa popanda mtendere sipangakhale chitukuko.
Iwo anati kumbali ya maboma amene adachita malire ndi mayiko ena, ntchitoyi ayigwire akakhazikitsa makomiti olimbikitsa mtendere komanso othetsa mikangano.
Gawo loyamba la ntchitoyi linayamba m’chaka cha 2022 yomwe inatha chaka chatha ndipo inaphunzitsa achinyamata komanso amayi m’ma boma a Mulanje ndi Mangochi, omwe ali m’malire ndi dziko la Mozambique.