Apolisi ku Kamuzu International (KIA) amanga a Lyndiwe Khembo Chihana, 46, powaganizira kuti anavulaza ogwira ntchito ku Ethiopian Airlines komanso apolisi awiri.
Ofalitsankhani ku polisi ya KIA, a Dorrah Chathyoka, akuti a Chihana Lachinayi anali pa ulendo opita m’dziko la United Kingdom kudzera munzinda wa Addis Ababa m’dziko la Ethiopia.
Mayiwa anakwera ndege ya mtundu wa Boeing 787, ndege ya Boeing 747 itakanika kunyamuka kaamba ka zovuta zina.
Koma zimene zinadabwitsa anthu, malinga ndi a Chathyoka, akuti a Chihana amakakamira kukhala mpando umene pamakhala ogwira ntchito mu ndege.
Captain oyendetsa ndegeyo anayitana apolisi kuti alowelerepo chifukwa ngakhale anawauza mayiwo kuti akakhale malo apamwamba mwaulele, iwo anakana ndikuyamba kutukwana ndi kumenya ogwira ntchito mundege.
Atatsika, a Chihana anakamenyanso mkulu wa Ethiopian Airlines ndipo Lachisanu lino akuyembekezereka kuti akayankhe mlandu odzetsa chisokonezo pamalo komanso kuvulaza anthu.
A Chihana, amene ndi namwino, amachokera pamudzi wa Mbenderana, kwa T/A Kasisi m’boma la Chikwawa.