Apolisi ku Chileka mu mzinda wa Blantyre amanga anthu anayi powaganizira kuti amatuma ana kuti adziwagulitsira malonda nthawi ya sukulu.
Ofalitsa nkhani ku Polisi ya Chileka, a Phillipo Jonathan, anati kutero ndi kuphwanya ufulu wa ana.
A Phillipo anaonjezeranso kuti amanga anthuwo potsatira kuchuluka kwa ana amene amapezeka akugulitsa malonda pa sitolo za ku Lunzu nthawi imene ndi ya sukulu.
Kutsatira izi, apolisi apulumutsa ana 42 ku m’chitidwe umenewu ndipo ena awatumiza kwa makolo awo.