Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

TISADULE MITENGO MWACHISAWAWA

Adindo a malo ochitira kafukufuku a Chitedze Research Station ku Lilongwe adandaula ndi mchitidwe wodula mitengo omwe akuti ukusokoneza ntchito zina za kafukufuku pa malopa.

Mkulu owona ntchito zakafukufuku pa Chitedze Research Station, a Lawrent Pungulani,  anena izi ku Chitedze mumzinda wa Lilongwe pomwe amabzyala mbande za mitengo.

“Anthu okhala mozungulira malo otetezedwa akuyenera kudziwitsidwa bwino za kasamalidwe kamitengo n’cholinga choti nawo atengepo gawo pobwezeretsa chilengedwe cha pa  malowa,” a Pungulani anatero.

Poyankhulaponso pa mwambowu, mkulu owona za kafukufuku ku unduna wa za ulimi,  a Grace Kaudzu, alimbikitsa a Malawi kutenga nawo gawo pobzyala mitengo m’malo otetezedwa ati kamba koti mitengoyi imapindulitsa munjira zambiri.

Ndipo Mfumu Chalenga , yati tsopano ili ndi udindo waukulu ophunzitsa anthu awo  ndi madera ozungulira za ubwino osamalira mitengo.

Malingana ndi a Pungulani, pa mwambowu, mbande za mitengo zoposa 20,000 ndi zomwe zinabzyalidwa.

Wolemba: Aisha Amidu.

 

#mbcmw

#mbcnewslive

#mbconlineservices

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Chipani cha ANC chikutsogola ku South Africa

Alinafe Mlamba

PMI READY TO ENGAGE GOVERNMENTS ON TOBACCO HARM REDUCTION

MBC Online

Awagwira komwe amabisala

Charles Pensulo
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.