Wachiwiri kwa nduna ya za umoyo, a Noah Chimpeni, atsindika kuti dziko la Malawi liri ndikuthekera koyendetsa ntchito za umoyo popanda thandizo la dziko la Amerika ndipo anthu asadere nkhawa.
A Chimpeni ayankhula izi ku Lilongwe kumene bungwe la Community St Egidio lomwe limathandiza nkhani za HIV, Khunyu komanso Khansa ya mmawere ndi yakhomo la chiberekero, likuchititsa mkumano ndi akuluakulu aza umoyo mmaboma komanso kuchokera kubugwe laku Germany loona zachitukuko mmaiko la BMZ.
M’modzi wa akuluakulu aku German pansi pabungweli wati nkofunika kugwiritsa bwino ntchito thumba la zaumoyo lomwe dziko lino lilinalo.
Mkulu wa Community of St. Egidio mdziko muno, a Mathambo William Lowole, wati sakubwerera mmbuyo ndi masomphenya okuza ntchito zabungweli kuti afikire anthu ochuluka.
Bungweli likugwira ntchito mmaboma osachepera asanu mdziko muno.