Bungwe la Tobacco Commission (TC) lati dziko lino likuyembekeza kukolora fodya pafupifupi makilogalamu 180 million, malinga ndi kafukufuku oyamba yemwe bungweli lachita.
Akuluakulu a bungweli amayankhula pamene iwo pamodzi ndi wachiwiri kwa nduna yaza ulimi, a Benedicto Chambo, amayendera ena mwa alimi a fodya m’boma la Machinga. Alimiwa akulima fodya wa bale komanso kampopi.
Poyankhula m’dera la mfumu Makoka kwa T/A Nyambi, a Chambo alangiza alimi a fodya kuti asalore mavenda kugula fodya kuti alimiwo apindule ndi ntchito yawo.
A Chambo ati zimakhala zopweteka ndi zomvetsa chisoni kuona mlimi akudzipereka pa ntchito yake koma opindula kukhala venda.
Komabe alimiwa ati nthawi zambiri amachita izi kamba kosowa mwayi wa ngongole, choncho mavendawa amawabwereka ndalama kuti adzabweze fodya.
Pamenepa alimiwa apempha boma kuti lifupikitse ndikufewetsa ndondomeko zopezera ngongole kuti adzitha kupeza ngongole za boma osati kwa venda.
Mchaka cha 2024, dziko lino linapeza makilogalamu 133 million a fodya.
Olemba: Beatrice Juma

