Phungu wadera la Blantyre City East, a John Bande, wapempha mafumu kuti akhale patsogolo poteteza zipangizo ndi katundu wa boma pomwe akulimbikitsa ntchito zachitukuko.
A Bande anena izi pa mwambo olonga a Horace Chilembwe kukhala Group Village Headman Nanthoka ku Machinjiri ku Blantyre.
Iwo anatchulapo malo a Machinjiri Chitukuko Centre pomwe boma likumangapo chipatala ndi sukulu ndi zina, kuti akufunika kuwateteza kuti anthu ena asalowelere.
Ena mwa athu omwe anali nawo pamwambowu ndi mlembi wamkulu ku unduna wa zachuma, a Betchani Tchereni, kudzanso anthu omwe akufuna kudzapikisana nawo pachisankho ngati phungu omwe ndi a Deus Sandram “Bwande”, Alex Chimwala komanso a Chisawa Mbewe.