Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Mipingo ithokoza okumba manda ku Area 18

Anthu asanu ndi atatu amene amakumba manda ku manda a Area 18, pansi pa Lilongwe City Council, alandira njinga komanso K250,000 aliyense ngati njira imodzi yowathokoza kaamba kogwira ntchito mokhulupirika pa nthawi yomwe matenda a COVID-19 anasowetsa mtendere m’dziko muno.

Omwe apereka ndi mtsogoleri wa Salvation for All Ministries, Apostle Clifford Kawinga, mogwirizana ndi m’busa Hamilton Yasin Gama, amene amatumikira pa Mvama CCAP mu nzinda wa Lilongwe.

A Josam Bikoziti, amene agwira ntchito yokumba manda ku Area 18 kwa zaka 31, ati ntchito yawo inali yowawitsa pakati pa 2020 ndi 2022, kotero anathokoza kaamba ka mphatso zimene apatsidwazi.

Iwo alandiranso sopo, mafuta ophikira komanso zitenje, mwa zina.

A Kawinga komanso a Gama ati pamene ena amakhala kutali ndi odwala kapena thupi la amene wamwalira ndi COVID-19, anthuwa anagwirabe ntchito yawo modzipereka, osalingalira za kuwopsa kwa COVID-19.

“Ndi anthu ofunikira kwambiri. Ndi anthu owoneka a pansi, koma ogwira ntchito yotamandika,” anatero a Kawinga.

Pamwambowu panafikanso mfumu ya nzinda wa Lilongwe, Councillor Richard Banda ndi mkulu wa zaumoyo ku khonsolo ya nzindawu.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

NGORA yati K1BN ithandiza mabungwe awo kudzidalira

Emmanuel Chikonso

COSOMA ipereka ndalama kwa oyimba

Simeon Boyce

Okhupha mnzake amugwira

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.