Amene anajambula kanema wa Belinda, gulu la Remnant Lions, ati ali ndi chikhulupiliro kuti kanemayu alimbikitsa atsikana kuti asamafooke pa maphunziro ngakhale atakumana ndi mavuto, kuphatikizapo kutenga pakati.
Otsogolera ntchito yojambula m’kanemayu, a Tionge Chisiza, ati aonetsetsa kuti seweroli lifikire aliyense, makamaka m’sukulu zakumudzi.
Iwo amayankhula izi Lachisanu madzulo atawonetsa kanemayu mu nzinda wa Lilongwe.
“Tikufuna aliyense yemwe ali ndi chidwi cholimbikitsa maphunziro aonere kanemayi,” a Chisiza anatero.
Kanemayu anamuonetsa kale munzinda wa Blantyre ndipo pali chikonzero kuti akamuonetsenso ku Mzuzu ndi ma boma ena.
Gulu la Remnant Lions analitsogolerako ndi malemu a Thlupego Chisiza.