Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Michael Usi, walimbikitsa anthu achipembedzo cha chisilamu kuti apitirize kukhala chitsanzo chabwino pa ntchito yolimbikitsa chikondi komanso kulolerana kudzera mu chiphunzitso cha chisilamu.
Dr Usi anena izi pa bwalo la Kasolo m’boma la Mangochi pamwambo wa mapemphero komanso chikondwelero cha Eid.
Iwo anati boma limayamika ntchito yomwe achipembedzo cha chisilamu amagwira polimbikitsa chikondi, umodzi komanso kugwira ntchito za chifundo.
“Mupitirize kukhala chitsanzo chabwino ndipo pemphelerani mtendere m’dziko muno pamene tikuyandikira chisankho pa 16 September chaka chino,” Dr Usi anatero.
Wapampando wa komiti yomwe inakonza mwambowu, Sheikh Ahmad Hussein, analonjeza kuti apitiriza kugwira ntchito limodzi ndi boma.
Olemba: Owen Mavula