Malawi Broadcasting Corporation
Entertainment Entertainment Local Music News Nkhani

Malinga Mafia wapepesa atachedwa ku Illusionz

Katswiri oyimba Dancehall, Malinga Mafia, wapepesa kwa okonda nyimbo zake kaamba kokanika kuyimba ku phwando lamayimbidwe la Illusionz lomwe likuchitikira pagombe m’boma la Mangochi.

Katswiriyu amayenera kutsekulira phwandoli Lachisanu madzulo, koma m’malo mwake, ma Blacks ndi amene anagwira ntchitoyi.

Malinga anachedwa ndi ola limodzi chifukwa iye pamodzi ndi oyimba ena anagwiritsa ntchito khomo lolowera gulu kuphwandoli.

“Zachitikazi likhale phunziro kwa omwenso akonza mwambowu, adzisiyanitsa khomo lolowera anthu odzayimba ndi odzaonelera kuti padzikhala dongosolo,” Malinga anatero.

Phwandoli ndi la masiku atatu. Oyimba akunja monga Eemoh ndi Dj Tira afika kale ndipo Dj Maphorisa ndi Kabza akuyembekezeka kuti afike lero.

 

Related posts

BAM champions sustainable finance to strengthen climate resilience

Chisomo Break

2nd Global Environment Facility (GEF) on Sustainable Forest Management Begins

Rabson Kondowe

265 Energy yamema kampani kuti zitsegule malo ogulitsa gasi

Mayeso Chikhadzula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.