Bungwe la Greenbelt Initiative Authority lapereka ntchito ya gawo lachiwiri lomanga malo a mthilira a Nthola-Ilola m’boma la Karonga kwa amene agwire ntchitoyi, a Kabiki and Partners, Sico Civils komanso a China Civil Engineering Construction Company.
Mkulu oona zomangamanga ku bungweli, a Snowden Kautsi, ati ntchitoyi ikuyenera kuyenda bwino chifukwa mavuto amene anakumana nawo mugawo loyamba achepa.
“Mavuto omwe tinali nawo kwambiri amakhudza ndalama koma pano boma laonjezera ndalama kuntchitoyi kuchoka pa K1 billion chaka chatha kufika pa K14 billion chaka chino,” a Kautsi anatero.
Mugawo lachiwiri lantchitoyi, akuyenera kupitiriza ntchito yomanga njira zotengera madzi kulowetsa m’minda, zipinda zosungira mpunga pa fakitale yogaya mpunga ya Nthola-Ilola, maofesi komanso kumaliza mpanda wa fakitaleyi.
Malo okwana mahekitala 357 mwamahekitala 1000 a Nthola-Ilola ndiamene adzayambe kutulutsa mpunga wa Kilombero ntchitoyi ikadzatha.
Olemba: Henry Haukeya