Bungwe la Transporters Association of Malawi lati kukonza msewu wa Mangochi-Makanjira kudzathandizanso kwambiri kulimbikitsa ntchito za mtengatenga ndi malonda pakati pa dziko lino ndi la Mozambique.
Mkulu wa bungweli, a Elliot Mussa, wanena zimenezi poyankhula ndi MBC Digital pamene boma latsimikiza kuti ntchito yokonza msewuwu iyambika posachedwa.
Iwo anaonjezeranso kuti msewu umenewu udzapangitsa kuti mayendedwe aphweke pakati pa mayiko awiriwa komanso kuti katundu, kuphatikiza mbewu, adzitha kunyamulidwa kuchokera ku Makanjira ndi kukafika mmalo ena mosavuta.
A Mussa anayamikiranso boma kaamba kochilimika pachitukuko chomanga komanso kukonza misewu yosiyanasiyana, zimene anati zithandiza kuti eni galimoto asamawononge ndalama zambiri pokonzetsa galimotozi, zomwe zimawonongeka pafupipafupi akamayenda m’misewu yosakhala bwino.
Boma likuyembekezera kuyambapo ntchito yomanga msewuwu kuyambira m’mwezi wa July potsatira kuvomereza kwa nyumba ya malamulo kuti boma libwereke $9.6 million kuchokera ku Kuwait Fund, zimene zili ndalama zowonjezera pogwira ntchitoyi.