Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Micheal Usi, ayamikira ndi kuthokoza mpingo wa Anglican pogwira ntchito ndi boma m’magawo osiyanasiyana a chitukuko.
Dr Usi anena izi pa bwalo la masewero la Silver ku Lilongwe pa mwambo wotsanzikana ndi Right Reverend Francis Frank Kaulanda yemwe ndi bishop wa chitatu wa Diocese ya Lake Malawi ya mpingo wa Anglican, amene akupuma pa ntchito.
Iwo ati mpingowu uli ndi udindo wothandizira anthu kukhala abwino chifukwa mavuto ena omwe dziko lino likukumana nawo, monga katangale, amachita ndi anthu a m’mipingo.
Dr Usi ati boma ndilokondwa ndi ntchito zabwino zomwe a Kaulanda agwira mothandizidwa ndi mpingo wa Anglican zomwe ati zafikira anthu ambiri m’dziko muno.
Apa Iwo ati boma ndi mpingo zili ndi mphamvu zomwe kuziphatikiza zikhoza kuthana ndi mavuto omwe dziko lino likukumana nawo.
Dr Usi ati boma ndi lodzipereka kugwira ntchito ndi mipingo pofuna kusintha kaganizidwe komanso kulikimbitsa makhalidwe abwino komanso chimvano zomwe ati nzothandiza kuti anthu akhale olimbikira komanso okonda dziko lawo.