Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Timakhulupilira mtendere – MCP

Chipani cha Malawi Congress (MCP) chati sichikhala nawo ku msonkhano waukulu wa chipani cha United Democratic Front (UDF) potsatira mphekesera yoti zipani zina zotsutsa zachita upo ofuna kuyambitsa zachisokonezo kaamba kakupezeka kwa chipanichi kumsonkhanowo.

Chikalata chomwe chipanichi chatulutsa ndipo wasainira ndi mlembi wamkulu, a Richard Chimwendo Banda, chipani cha MCP chayamikira chipani cha UDF kaamba ka ganizo lake lowaitana ku msonkhano wake waukulu.

Iwo ati aka ndikoyamba kuti chipani cha UDF chiyitane chipani cha MCP ku msonkhano waukulu kwa zaka makumi atatu zomwe dziko lino lakhala liri mu ulamuliro wa zipani zambiri.

Komabe iwo mu chikalatacho ati ngakhale chipani cha MCP chinali chofunitsitsa kukapezeka pamsonkhanowo, chipanichi sichipezekako pofuna kulimbikitsa bata ndi mtendere zitamveka kuti azipani zina zotsutsa akuganiza zokasokoneza, komanso kupereka mpata kuti chipani cha UDF chichititse msonkhano wake mwamtendere.

Pamenepa, chipani cha MCP chafunira zabwino chipani cha UDF pomwe chichititse msonkhano wake waukulu kuyambira lachitatu likudzali.

 

Olemba: Charles Pensulo

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Tiyeni tiphunzirepo pa moyo wa Dr. Chilima – St Patrick’s Parish

MBC Online

‘Nyumba yamalamulo ya ana ikufunika thumba lapadera’

Lonjezo Msodoka

Local govt ministry tips NGOs to engage district councils for development

Charles Pensulo
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.