Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Michael Usi ati ndi okhumudwa kuti ena mwa aphungu anyumba ya malamulo sakuonetsa chidwi chogwiritsa ntchito ndalama zonse zomwe zili mu dongosolo la Community Development Fund (CDF).
Dr Usi amanena izi mu ofesi ya a Bwanamkubwa a m’boma la Thyolo a Hudson Kuphanga.
A Kaphanga amafotokoza kuti zina mwa ndalama zomwe aphunguwa amalandila m’madera a aphungu, sazimvetsa komanso samazigwiritsa ntchito zonse pa chitukuko.