Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Micheal Usi, afika m’dziko muno mawa atakhala nawo pa mwambo olumbilitsa mtsogoleri wa tsopano wa dziko la Mozambique, a Daniel Chapo.
A Chapo alowa m’malo mwa a Felipe Nyusi amene nthawi yawo yokhala pa udindowu inatha kutsatira pamene analamulira dzikolo maulendo awiri.
Chipani cholamula bomalo, cha FRELIMO chakhala chikulamulira dzikolo kuyambira pamene dziko la Mozambique linalandira ufulu odzilamulira m’chaka cha 1975.
Dr Usi akuyembekezeka kufika m’dziko muno nthawi ya 2:35 masana kudzera pa bwalo la Chileka munzinda wa Blantyre.