Apolisi ku Mulanje akufunafuna Joseph Louis yemwe akumuganizira kuti wapha Brian Mwaliwa wazaka 30.
Louis anapha Mwaliwa atamupeza akuchita zadama ndi mkazi wake. Zadamazi amachitira mnyumba mwa Louis momwemo.
Mneneri wapolisi ku Mulanje, a Innocent Moses, ati Mwaliwa anali pa chibwenzi cha mseri ndi mkazi wa Louis.
A Moses ati patsikulo, a Louis anatsanzika mkazi wao kuti akupita kumsika kukagulitsa zovala za kaunjika, bizinesi yomwe amachita nthawi zonse. Apa mkaziyo anaimbira foni Mwaliwa nkumuza kuti mwamuna wake wachoka ndipo abwere kunyumbako kuti azasangalale.
Awiriwa ali mkati mosangalala a Louis anabwelera kumsika kuja ndipo anawapezelera awiriwo ali mchikondi. Apa, a Louis anabaya Mwaliwa ndi scissors pa mimba. Mwaliwa anayesetsa kuthawa koma anthu anamupeza pamalo ena atafa. Izi zachitika mmudzi wa Watheya, Mfumu yaikulu Juma ku Mulanje.