Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera akuyembekezeka kukambirana ndi kampani zoona za sitima zapamadzi ku Germany kuti athandize kuyambitsa ntchito za maulendo pa nyanja ya Malawi pothana ndi mavuto amayendedwe panyanjayi.
Nduna yoona nkhani zakunja a Nancy Tembo anena izi pomwe Dr Chakwera akuyembekezeka kufika ku Frankfurt ku Germany lachitatu kuchokera ku Italy komwe akakambilane ndi makampaniwa.
Iwo ati ali ku Germany, Dr Chakwera akambirana ndi kampaniyi za maulendowa poonjezela kukambirana zankhani ya magetsi asanakumane ndi mtsogoleri wa dziko la Germany.