Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Amumanga ataba mu kachisi

Apolisi ku Lilongwe amanga mwamuna wazaka 44, Patrick Zgambo, pomuganizira kuti waba zipangizo zoyimbira za ndalama pafupifupi K3.5 million za tchalitchi chotchedwa Time of God.

Mneneri wapolisi ku Lilongwe, Hastings Chigalu, wati mkuluyo, yemwe amachokera m’mudzi wa Mzikubola, Mfumu yaikulu Maulabo m’boma la Mzimba, amagwira ntchito yolondera patchalitchicho.

A Chigalu ati apolisi agwira mkuluyo m’bandakucha wa pa 15 May mu msewu wa Kamuzu Procession ku Lilongwe komweko pomwe anabisa zinthuzo mu zikwama.

Iye anaulula kuti waba zipangizozo ku tchalitchicho.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Ophunzira apindilana ndebvu mkamwa

MBC Online

Osewera mpira wa asungwana akusokonekera

MBC Online

Thupi la Malemu Hope Chisanu lafika m’dziko muno

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.