Malawi Broadcasting Corporation
Agriculture Development Local Local News Nkhani

Boma lakonzanso ndondomeko ya chuma cha ADMARC

Unduna wa zamalimidwe wati wakonza ndi kuunikanso ndondomeko ya chuma yomwe anaikonza kuti agulire chimanga chaka chino.

A Geoffrey Mamba, amene ndi mlembi ku undunawu, ati izi adapanga lachitatu pamene komiti yoona za Chakudya komanso za ulimi yaku nyumba ya malamulo mu mzinda wa Lilongwe inaona kuti thumba la ndalama zogulira chimanga lidali lochepa.

“Timayenera tigule matani 5,000 a chimanga cha chaka chino, ndipo m’malo mwake tigula ma tani 20000. Ndalama ndi yomweyo K40 billion tangochotsa zina zomwe zimayenera kuti zipite ku ntchito zina,” a Mamba anafotokoza.

A Welani Chilenga, amene amatsogolera komiti yaku nyumba yamalamuloyo, anayamikira boma kaamba kogwiritsa ntchito zomwe adakambirana.

“Aka ndi koyamba chiyambireni kukhala m’makomiti kuona zokambirana za pamwamba zotere zokhudza chakudya ndi ulimi,” a Chilenga anatero.

ADMARC yatapa K21.8 Billion m’thumba la K40 Billion pamodzi ndi bungwe la National Food Resilience Agency (NFRA), yomwe anayipatsa K12 Billion kuti igule chimanga chokwana ma tani 34000.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

CHAKWERA HOMEBOUND

MBC Online

Chipiku increases sponsorship for CRFA

Romeo Umali

CHINA PLEDGES CONTINUED SUPPORT TO MALAWI

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.