Kuli chisangalalo chokhachokha mmudzi mwa Mzonde komwe mtsogoleri wadziko lino, Dr Lazarus Chakwera, akukhazikitsa ntchito yomanga misewu, pansi pantchito ya Millennium Challenge Account.
Anthu ochuluka afika pa bwalo la Mzonde pomwe aikapo kanema yayikulu kuti akhoza kutsatira mwambo onse.
A Lettina Kalumbi a mmudzi mwa Tsabango ndi m’modzi mwa anthu mazanamazana omwe afika kudzaonelera kutsekulira kwa ntchitoyi ndipo akuti iwo ndi anzawo ochuluka ayenda makilomita oposa 5 kuchokera kwa Msundwe kudzaona kukhazikitsidwa kwa ntchitoyi, ati kuti akhale ndi umboni kuti yayambadi.
A Kalumbi akuti ndionyadira poti msewu umenewu ndiofunika pokagulitsa mbewu zawo, yomwe ndi ntchito yawo ya tsiku ndi tsiku.