Malipoti akusonyeza kuti mtsogoleri wambali ya aphungu otsutsa boma kunyumba yamalamulo, a Kondwani Nankhumwa, akhazikitsa chipani chatsopano chotchedwa People’s Development Party (PDP).
Malinga ndi kalata yomwe ayibweretsa poyera kudzera patsamba lawo la mchezo, chipanichi chichititsa msonkhano wa atolankhani posachedwapa kumenenso chidzasonyeze kumtundu wa aMalawi atsogoleri ake ongogwirizira ma udindo.
A Nankhumwa, omwe ndi phungu wadera la pakati m’boma la Mulanje, adachotsedwa m’chipani cha Democratic Progressive (DPP) miyezi yapitayo.