Anthu ochuluka akhamukira pabwalo la Mzonde kwa mfumu yaikulu Kalolo ku Lilongwe komwe mtsogoleri wadziko lino, Dr Lazarus Chakwera, pamodzi ndi mkulu wa Millennium Challenge Corporation, Madam Alice Albright, akhazikitse ntchito yokonza misewu pansi pa Millennium Challenge Account – Malawi II (MCA-M).
Wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino, Dr Saulos Chilima, nawonso alinawo kumwambowu.
Malinga ndi mkulu yemwe akutsogolera ntchitoyi kuno ku Malawi, a Dye Mawindo, akangotsekulira zonse zochitika ziyambika.
Ntchitoyi, yomwe ndi ya ndalama zokwana $300 million, ayigwira kwa zaka zisanu.