Apolisi ku Zomba amanga a Jaru Kambanga, 36 ndi a Patrick Bwanali, 31 powaganizira kuti anagwililira komanso kuba katundu wina pa malo ogona atsikana a sukulu ya ukachenjede ya Domasi Institute.
A Patricia Sipiliano, amene ndi ofalitsankhani wa Polisi ya Zomba, ati awiriwa pamodzi ndi enanso awiri omwe sakupezeka, adatchola ndi kulowa m’zipindazo atanyamula zida zochititsa mantha kenako anaba katundu wambiri, kuphatikizapo ma foni ndi zikwama.
A Sipiliano anaonjezerapo kuti atamaliza kubako, anthuwa anagwililira atsikana ena kenako anathawa.