Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera pamodzi ndi Madame Monica Chakwera, watsogolera mtundu wa aMalawi powona nkhope ya wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, malemu Dr Saulos Chilima ku Nyumba ya Malamulo ku Lilongwe.
Pambuyo pa Dr. Chakwera, a Mary Chilima amene ndi mkazi wa malemuwa, nawo awona nkhope ndikutsanzikana ndi Dr. Chilima.
Mtsogoleri wakale wa dziko lino, a Joyce Banda komanso Chief Justice opuma a Richard Banda, nawo apereka ulemu wawo omaliza kwa Dr Saulos Klaus Chilima.
A Khumbo Kachali, omwe anakhalapo wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, nawonso apereka ulemu wawo omaliza.
Mkulu wama Judge, a Rezin Mzikamanda komanso mkulu wa asilikali a nkhondo a MDF, General Paul Velentino Phiri ndi nduna zonse zaboma nawo apereka ulemu wao kwa Dr. Chilima.
Mmene zateremu ndiye kuti aMalawi akhala ndi mwayi opereka ulemu wawo, tsiku lonse mpaka 8 koloko madzulo ano.
Olemba: Isaac Jali & Mirriam Kaliza