Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

“Palibe atafe ndi njala” — Kunkuyu

Nduna ya zofalitsa nkhani yemwenso ndi m’neneri wa boma, a Moses Kunkuyu, ati mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera watsindika kuti palibe munthu amene atafe ndi njala m’dziko muno.

A Kunkuyu afotokoza izi pa msonkhano wa atolankhani mu mzinda wa Lilongwe, kumenenso anati boma lapeleka ndalama zokwana K50,000 ku makomo 783,000.

A Kunkuyu atinso ndalama yokwana K43 billion ndi imene Boma lagwiritsa ntchito pogulira chimanga kudzera ku ofesi ya mtsogoleri wa dziko lino komanso ku DoDma.

Izi zili chomwechi kutsatira report lomwe lidatuluka loti anthu 4.4 million atha kukhudzidwa ndi njala.

Izi ati ndi malinga ndi ng’amba komanso Cyclone Freddy, mwa zina zambiri.

#MBCOnlineServices
#inspiringthenation

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Mamembala a COMSIP alimbikitsa ukhondo m’misika

Doreen Sonani

Scorchers lero imwemwetera

Paul Mlowoka

Council officials urged to promote rights of persons with disabilities

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.