Nduna yazofalitsa nkhani , a Moses Kunkuyu, ati mtsogoleri wa dziko lino, Dr. Lazarus Chakwera, alamula kuti lolemba likudzali, limene lili tsiku loyika mmanda ku Ntcheu yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko, malemu Dr Saulos Chilima, likhale tsiku la tchuthi.
Iwo ati cholinga chake ndikufuna kuti aMalawi athe kulira maliro a Dr. Chilima.
A Kunkuyu alongosola izi kumsonkhano wa olembankhani kunyumba yamalamulo.
Mmau awo, iwo ati ku mwambowu kukapezekanso akuluakulu osiyanasiyana ochokera kunja kwa dziko lino monga ku Tanzania, Botswana ndi Mozambique.
Olemba Mirriam Kaliza