Bambomfumu apa Parish ya St Patrick’s mu mzinda wa Lilongwe, a Henry Zulu, alangiza Akhristu m’dziko muno kuti atengere chitsanzo chabwino cha moyo wa wachiwiri kwa Prezidenti wa dziko lino, malemu Dr Saulos Chilima.
Bambo Zulu anati Dr Chilima anali mkhrisitu odzipereka, olimbika pa ntchito za Chauta komanso pa ntchito zachifundo, zomwe anthu akuyenera kuphunzirapo.
Naye Bishop – mthandizi wa Archdiocese ya Lilongwe ya mpingo wa Katolika Bishop Vincent Mwakhwawa wati pamene aMalawi ali osweka mitima kaamba ka imfa yodzidzimutsayi, nkofunika ayang’ane kwa Chauta ndikulimbikitsa bata ndi mtendere komanso umodzi.
Wapampando wa Akhristu onse pa St. Patrick’s Parish, Dr Matthews Mtumbuka, anati malemu Dr Chilima amakhala bwino ndi anthu mosatengera udindo wa munthu ndipo amadzipereka pa ntchito za mpingo monga adaachitira panthawi imene ankamanga tchalitchi chatsopano, ponena kuti adathandizapo kwambiri.
President Dr Lazarus Chakwera, mayi wa fuko la dziko lino, mkulu wama Judge, Rezin Mzikamanda, nduna zaboma ndi ena mwa akuluakulu omwe anali nawo pa misayo.
Olemba: Isaac Jali