Bungwe la Competition and Fair Trading Competition (CFTC) lapereka zigamulo 90 pamadandaulo omwe analandira okhudza makampani komanso masitolo omwe samatsatira malamulo oyenera ochitira malonda.
Mkulu wa bungweli, a Lloyds Vincent Nkhoma, awuza olembankhani mu mzinda wa Lilongwe kuti theka la madandaulo omwe analandira anali okhudza shuga yemwe anthu amagula mokwera mosiyana ndi mtengo wake ovomerezeka.
Iwo ati madandaulowo awatumiza ku ofesi ya mkulu ozenga milandu m’boma kuti atsekulire milandu makampani okhudzidwawo.
Mwa ina mwa milanduyo ndi ya Afriplus Steel Malata omwe analandira ndalama zolipira malata koma osapereka kwa ma kasitomala ake.
Chonchobe Shop yomwe imagulitsa shuga pa mtengo okwera nthawi imene katunduyi amasowa chaka chino, pamodzi ndi Rosina Enterprises kaamba kosunga shuga osamugulitsa pomwe ogula amamufuna komanso Simama General Dealers, mwa ena.
A Nkhoma ati aka kakhala kotsiriza kuti azitumiza nkhani zotere kwa ofesi yamkulu ozenga milandu m’boma kaamba koti lamulo latsopano loonetsetsa kuti ntchito zamalonda zikuchitika motsatira malamulo likuwapatsa mphamvu zopereka chindapusa.
Lamulo latsopanoli linayamba kugwira ntchito mwezi wathawu.