Ngati njira imodzi yofuna kupititsa patsogolo ntchito za milingo mdziko muno, bungwe loona za milingo la Malawi Bureau of Standards lati linakhazikitsa ndondomeko yopereka mphatso ya ndalama zokwana K50,000 kwa yemwe angawatsine khutu zamchitidwe ogulitsa kapena kupanga katundu mosatsatira malamulo a bungweli.
Izi zadziwika pomwe bungweli linachititsa maphunziro osula atolankhani za kalembedwe kankhani zokhudza milingo ku Salima.
Mkulu wa Bungweli, a Benson Thole, ati zina mwanjira zomwe anthu angatsate ndi monga kulemba kalata kwa mkulu wa bungweli kapena kuimba foni pa 462 kapena 842.
A Thole anati kugulitsa kapena kupanga katundu osayezedwa mlingo ndi mlandu waukulu kaamba koti khalidwe lotere limapereka chiopsezo kumiyoyo yawanthu
Olemba: Mphatso Tebulo