Bungwe la Centre for Social Accountability & Transparency (CSAT) lati ndi koyenera kuti olembankhani azidziwa komanso kutsatira bwino momwe nyumba ya malamulo (Parliament) imagwilira ntchito zake.
M’modzi mwa akuluakulu ku bungweli a Moffat Phiri, ayankhula izi mu mzinda wa Lilongwe pa maphunziro a atolankhani okhudza kalembedwe ka nkhani ya kunyumbayi komanso zalamulo lothandiza kupeza uthenga mosavuta (ATI).
“Atolankhani ali ndi ntchito yaikulu yodziwitsa anthu zazomwe zikuchitika ku nyumba ya malamulo ndi kufalitsa kwa anthu kuti athe kutenga gawo pazitukuko zam’madera awo,” anatero a Phiri.
Kufikira pano, a CSAT aphunzitsa atolankhani oposa makumi atatu kuchokera kunyumba zikuluzikulu zolemba komanso kuwulutsa mawu ndi zam’madera zomwe.