Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Bungwe la MEC lalowa mu mgwirizano obwerekana katundu ndi bungwe la ECZ

Bungwe loyendesa chisankho m’dziko muno la MEC lalowa mu m’gwirizano obwerekana katundu oyendetsera chisankho ndi bungwe loyendesa chisankho la ECZ la m’dziko la Zambia.

Ngati mbali imodzi ya mgwirizanowu, MEC yabwereka majenereta 1,500 kuchokera ku ECZ kuti adzathandizire pa ntchito yakalembera wa chisankho cha chaka chamawa.

Malinga ndi chikalata chomwe atulusa a MEC, majeneretawa ndiofunika kwambiri chifukwa adzathandizira kuti ntchito yakalembera idzayende mopanda zotsamwitsa.

Bungweli lati majeneleta 1,500 wa afika m’dziko muno pa 8 September, 2024 kudzera m’boma la Mchinji.

Bungwe la MEC latinso kubwerekana katundu oyendetsera chisankho pakati pa maiko a mu SADC sizachilendo chifukwa mchaka cha 2014, dziko la Malawi linabwereka nyali komanso ma tenti kuchokera m’maiko a Zimbabwe komanso Zambia.

Ndipo mchaka cha 2020, bungwe la ECZ nalo linabwereka mageneleta 2,200 kuchokera ku bungwe la MEC omwe anagwiritsa ntchito pa chisankho cham’chaka cha 2021 cha m’dzikolo.

 

Olemba Alufisha Fischer

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

We are a people who love and respect one another — Chakwera

MBC Online

Govt hails elderly rights promotion efforts

Secret Segula

Six people killed in Dedza road accident

Sothini Ndazi
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.