Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Wagona ndi mwana komanso kuponya zithunzi zake zolaula pa Facebook

Apolisi ku Blantyre amanga Clever Makina wazaka 25 pomuganizira kuti wagona ndi mtsikana wazaka 16 komanso kutumiza kanema yowonetsa ziwalo zobisika za mtsikanayo pamasamba a mchezo a Facebook.

Wachiwiri kwa mneneri wapolisi ku Blantyre, Mary Chiponda, wati Makina anatsegula Facebook yake yabodza pomwe amadziwonetsa ngati ndi mkazi.

Kenako anayamba kucheza ndi mtsikanayo, yemwe amaganiza kuti akucheza ndi munthu wa mkazi.

Tsiku lina, Makina anauza mtsikanayo kuti akufuna kumuthandiza monga munthu wachifundo ndipo anamupempha kuti akakumane kumalo ena ogona alendo ku Lunzu munzinda womwewo wa Blantyre.

Mtsikanayo atalowa mu chipinda chomwe munali Makina, anazindikira kuti munthuyo ndi wamwamuna ndipo Makina anaumiriza mtsikanayo kuti amujambule kanema ali maliseche ndikumuuza kuti ayitumiza pa Facebook ngati samupatsa ndalama zokwana K400,000, apo ayi agone naye.

Popeza mtsikanayo analibe ndalamazo, anavomera kugona ndi mwamunayo ngakhale kuti pamapeto pake anazitumizabe pa Facebook.

Makina wavomera kuti anachitadi izi.

 

Olemba Charles Pensulo

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Five men behind bars over ESCOM property vandalism

MBC Online

Veep calls for immediate Forest Policy reforms

McDonald Chiwayula

Centenary Bank partners with Tourism Ministry

Yamikani Simutowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.