Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

‘Miyoyo yathu yasitha’

Anthu ena omwe apindula ndi mtukula pa khomo m’boma la Karonga ati ndondomekoyi yasintha miyoyo yawo pa chuma.

Anthuwa anena izi pomwe mlembi ku unduna owona kuti pasamakhale kusiyana pa ntchito pakati pa amayi ndi abambo, chitukuko cha kumudzi ndi chisamaliro cha anthu, a Nwazi Mnthambala amayendera anthuwa kuti awone momwe ndondomekoyi ikuthandizira.

M’modzi mwa opindulawa, mayi Tionge Mwandovie, omwe akhala pansi pa ndondomekoyi kuchokera mchaka cha 2018, ati moyo wawo pano unasintha pomwe akwanitsa kumanga nyumba, kugula njinga ya moto, mbuzi komanso ng’ombe.

Nawo a Zaire Mkandawire omwe amapanga wine kuchokera ku masawu, athokoza boma powapatsa maphunziro komanso ndalama zoyambira bizinesi yawo kudzera ku Comsip.

Mmau awo, a Mnthambala anati ndi okondwa kuti ndondomeko ya mtukula pa khomo ikusintha miyoyo ya anthu.

Olemba: George Mkandawire

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Parliament passes the Cannabis Amendment Bill

MBC Online

Mera lifts ban on use of jerry cans

MBC Online

Mwang’onga Mkandawire to be laid to rest today

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.