Apolisi ku Nathenje ku Lilongwe amanga Ivy Elinati pamodzi ndi mwamuna wake Mphatso Nalinde onse azaka 25, powaganizira kuti apha mwana wawo wazaka ziwiri pofuna kulemera. Nalinde ndi bambo womupeza mwanayo.
Mneneri wapolisi ku Lilongwe Hastings Chigalu wati banjalo linapita kwa sing’anga wina ku Mozambique kuti likufuna kulemera. Ndipo sing’angayo anauza banjalo kuti liphe mwana wawo ndikupita ndi thupi lake ku Mozambique’ko.
Banjalo litapha mwanayo pomupotokola khosi, linaimbira foni sing’angayo kuti likubwera ndi thupilo. Koma akuti sing’angayo anawauza kuti asabwerenso kamba koti sanatsatire njira zina popha mwanayo.
Kenako banjalo linabwelera ndi thupi la mwanayo kwao ndikunamiza anthu kuti wamwalira mwadzidzidzi, zomwe anthuwo sanakhutire nazo mpaka anawakakamiza ndikuwulura zoona zake.
Ivy Elinati ndi wa mmudzi wa Chimbwala T/A Mlonyeni ku Mchinji,pomwe Mphatso Nalinde ndi wa mmudzi wa Chikuwa, T/A Chitekwere ku Lilongwe.