Ndalama zokwana K80.4 million ndi zomwe zapezeka pa masewero amu ligi ya TNM apakati pa matimu a FCB Nyasa Big Bullets komanso Mighty Mukuru Wanderers omwe aseweredwa loweruka masana pabwalo la Kamuzu.
Matimu a Wanderers komanso Bullets atenga K16.7 million timu iliyonse kuchoka pa ndalamayi (K80.4 million)
Chaka chatha, pamasewero ngati omwewa ndalama pafupifupi K67.5 million ndi zomwe zinapezeka.
Masewerowa athera 1-1 pomwe Wanderers inagoletsa kudzera mwa Isaac Kaliati ndipo Bullets inagoletsa kudzera mwa Patrick Mwaungulu.
Wolemba Praise Majawa.