Boma lathetsa mulandu wa anthu atatu omwe anawamanga chifukwa chosokoneza mdipiti wa mtsogoleri wa dziko lino pa HHI mu mzinda wa Blantyre.
Mkulu oimira boma pa milandu, a Masauko Chamkakala, watsimikiza zankhaniyi polankhula ndi wailesi za MBC.
Anthu atatu omwe amawazenga mulanduwu, a Pearson Chimimba a zaka 48, a Hector Ndawala a zaka 38, komanso a Lucy Namba a zaka 35, anawamanga patapita masiku angapo, anthu omwe anali pa maliro ndipo amachokera dera lina ku Ndirande ndipo amapita kukaika zobvuta kumanda a HHI, atalimbana ndi apolisi a pamsewu kuti adutse msewu pa malowa.
Mtsogoleri wa dziko lino anali paulendo opita ku Chileka kukakwera ndege kupita ku Democratic Republic of Congo (DRC) pamene anthuwa anachita chisokonezochi.
#mbcnewslive
#mbconlineservices
#mbcnewslive