Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

FMB Capital Holdings yapanga phindu lokwana K137.8 billion

Gulu la kampani la FMB Capital Holdings lomwe liri ndi banki ya First Capital Bank (FCB) kuno ku Malawi lapanga phindu lokwana $78.7 million zomwe ndi (K137.8 billion) mu chaka chatha.

Izi ndi malinga ndi kalata yazachuma yomwe gululi latulutsa ndipo yasayinidwa ndi wapampando wa guliri a Terence Davidson komanso m’modzi mwa akulu akulu ake a Busisa Moyo.

Kupatulako ku Malawi, FMB Capital Holdings iri ndi kampani zachuma ku Botswana, Mozambique, Zambia, Zimbabwe komanso Mauritius.

FMB Capital Holdings yati phinduli lapezeka kamba ka mfundo zabwino zachuma zomwe akugwiritsa ntchito.

Gululi lati mwa phinduli, anthu amene ali ndi masheya mu kampaniyi agawana (dividend) $10.6 million yomwe ndi K18.5 billion.

Related posts

Zikhale urges Kasungu residents to register for 2025 elections

Romeo Umali

Solar-powered irrigation scheme excites community in Zomba

Romeo Umali

Invest your money — Sendeza

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.