Apolisi ya Nathenje m’boma la Lilongwe amanga a Luwashi Bakali, 26, powaganizira kuti apha mwana omupeza wazaka ziwiri.
Izi zachitika m’mudzi wa Kawale kwa mfumu yaikulu Mazengera m’bomalo, malinga ndi ofalitsa nkhani zapolisi ya Lilongwe a Hastings Chigalu.
A Chigalu ati mayi wamwanayo anapita ku kasamba ndipo pobwelera anapeza mwanayo atakomoka panja pa nyumba yawo ndipo iwo pamodzi ndi a Bakali anathamangira naye mwanayo ku chipatala cha Nkhoma Mission kumene anamwalira akulandira thandizo.
Koma kafukufuku wa chipatala anasonyeza kuti mwanayo wafa kaamba kovulala mkati mwa thupi lake kaamba komumenya.
Kutsatira izi, anthu ena anawatsina khutu apolisi chifukwa amaganizira kuti bamboyo wapha mwanayo chifukwa choti akhala akumuona akuzunza komanso kumenya mwankhanza mwanayo kuchokera pamene anakwatira mayi ake.