Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wapempha aMalawi kuti agwirizane ndi kuyenda limodzi ndi anthu omwe ali ndi chidwi chofuna kumanga dziko lino kuti chitukuko chipite patsogolo.
Dr Chakwera anena izi pa bwalo la pasukulu ya pulaimale ya Hannock Msokera ku Kasungu pa mwambo wokondwelera kuti mpingo wa African Methodist Episcopal Church wakwanitsa zaka 100 ukugwira ntchito zake mdziko muno.
Mtsogoleri wa dziko linoyu wati pali anthu ena omwe mmalo mothandiza kumanga dziko lino ndi kuona zabwino akupasula ndipo wapempha a Malawi kuti atangwanike pogwirizana ndi anthu omwe athandize kumanga dziko lino monga momwe a Hannock Msokera anachitira.
A Chakwera ati dziko lino liri ndi vuto loiwala ndi kunyoza komwe tachokera koma watsindika kuti mpingowu ndi ofunika ndipo nkofunika kuwakumbukira malemu a Hannock Msokera poti ati ndi maziko a ufulu wa dziko lino mu mbiri ya dziko lino.
Iwo ati mpingowu unathandiza Dr Hastings Kamuzu Banda kukapeza maphunziro a pamwamba Ku America zomwe ati zinabweretsa maziko a chitukuko cha chuma cha dziko lino komanso maziko a ufulu omwe anthu akusangalala nawo mdziko muno.
Mmawu ake, mkulu wa mpingowu kuno ku Malawi, a Manuel Chamamba, athokoza Dr Chakwera potsata m’mapazi a Dr Banda, polemekeza mpingowu. Iwo ayamikiranso mtsogoleri wa dziko lino pa ntchito za chitukuko monga zotukula migodi, ulimi ndi zokopa alendo zomwe akugwira komanso polimbana ndi mavuto omwe dziko lino likukumana nalo.
Mpingowu anaukhazikitsa mdziko muno mchaka cha 1924 ndipo umathandizira boma m’magawo a zaumoyo komanso zamaphunziro.