Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Dr Chakwera adzudzula mchitidwe wa chidodo pa ntchito

Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, walangiza atsogoleri a ntchito zosiyanasiyana kuti adzikhala anthu opilira, owonetsa chitsanzo chabwino nthawi zonse komanso kugwira ntchito mwachangu pofuna kuti dziko lino litukuke.

Dr Chakwera amalankhula zimenezi ku Bingu International Convention Centre ku Lilongwe pa msonkhano otchedwa Dynamic Leaders and Gatekeepers Forum.

Iye anati m’dziko muno muli khalidwe lina loyipa lomwe limachedwetsa chitukuko monga chidodo pochita zinthu ndipo anapempha aMalawi kuti asinthe machitidwe azinthu.

Poyambilira, mkulu wa Malawi School of Government, a Asiyati Chiweza, anapempha makolo kuti akhale patsogolo kulangiza ana kukhala a ulemu komanso olimbika pa ntchito.

A Chiweza ati ngakhale kuli zinthu zamakono monga lamya za m’manja, sibwino kugwiritsa ntchito zimenezi molakwika pofalitsa zina zopanda umboni komanso ndicholinga choyipitsa mbiri ya ena.

A Daudi Suleman, amene ndi mkulu wa Malawi Communications Regulatory Authority, anathilirapo ndemanga pa momwe zikuyendera ntchito za lamya za mmanja ponena kuti anthu 34 mwa 100 alionse amagwiritsa ntchito internet ndikutinso anthu ambiri ali ndi phone za mmanja.

Komabe iwo anati bungwe lawo ligwira ntchito yozindikiritsa anthu kagwiritsidwe ntchito koyenera ka lamya za manja kuti zisakhale zida zofalitsira bodza ndikuyipitsa ena.

Poyambilira penipeni, m’busa Zacc Kawalala wa mpingo wa World Alive watsindika kufunika koti mMalawi aliyense azindikire kuti kutukula dziko si udindo wa boma lokha, koma kudzipereka kwa aliyense.

 

Wolemba: Isaac Jali

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Chakwera calls for collective effort in the business sector

MBC Online

‘Adolescents should have access to sexual and reproductive health services’

MBC Online

Pali kusintha kwina pa programme — Kunkuyu

Beatrice Mwape
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.