Prezidenti wakale wadziko lino, Professor Peter Mutharika, wabwerera kuno kumudzi lero masanawa.
A Mutharika, omwenso ndi mtsogoleri wachipani chotsutsa cha Democratic Progressive, afika kuno kumudzi kudzera kubwalo landege la Chileka munzinda wa Blantyre.
Poyambirira, akuluakulu a chipanichi adatsutsa zoti a Mutharika ali m’dziko la South Africa pomwe wayilesi ya MBC idafotokoza zakuchoka kwa mtsogoleriyu.
Mmneneri wachipani cha DPP, a Shadreck Namalomba, adakanitsitsa zoti a Mutharika achoka m’dziko muno kufikira pomwe mlembi wamkulu wachipanichi, a Peter Mukhito, anatulutsa kalata yovomereza kuti a Mutharika alidi kunja kwa dziko lino.
Panali mphekesera yoti a Mutharika amalandira thandizo la mankhwala m’dziko la South Africa ngakhale kuti chipanichi chimati apita kukagwira ntchito zina.
A Mutharika, omwe ali ndi zaka 86, akhala m’dziko la South Africa kwa sabata ziwiri.


